MACRA IBWERETSA MAKINA OWUNIKA LAMYA ZOJUDULA M’DZIKO MUNO
Bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) lati makina omwe bungweli likufuna libweretsa m’dziko muno omwe adziwunikila ndikulora lamya zokhazo zomwe zinapangidwa mwaukadaulo ndieni ake kugwira ntchito, ndipo izi zithandidzira kuthetsa ena mwa mavuto omwe amadza kamba ka lamya zojudula.
Izi zayankhulidwa ndi mkulu wa bungwe la MACRA a Daud Suleman pasukulu ya ukachenjede ya MZUNI pomwe amaphunzitsa ophunzira apasekulupa zambiri zokhudza bungweli.
Malingana ndi a Suleman ati ophunzira amagwiritsa ntchito zipangizo za intaneti,lamya komanso ma kompyuta m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku ndipo ndizofunikila kuphunzitsa ophunzirawa zambiri zokhudza ufulu omwe ophunzira alinawo akamagwiritsa ntchito intaneti.
Mkulu ogwilizira udindo wa nthambi ya Open for Distance and E-learning Dr. Lydia Kishindo Mafuta ati maphunzirowa ndiothandiza kwambiri chifukwa awaphunzitsa ophunzirawa zomwe amaphunzira mkalasi ndipo atha kuzagwiritsa ntchito upangiliwu m’tsogolo akamadzagwira ntchito.
Wolemba Salomy Chisi.